Main pages

Surah Al-Qari'ah ( The Striking Hour )

Chewa

Surah Al-Qari'ah ( The Striking Hour ) - Aya count 11

ٱلْقَارِعَةُ ﴿١﴾

Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)!

مَا ٱلْقَارِعَةُ ﴿٢﴾

Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani?

وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا ٱلْقَارِعَةُ ﴿٣﴾

Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)?

يَوْمَ يَكُونُ ٱلنَّاسُ كَٱلْفَرَاشِ ٱلْمَبْثُوثِ ﴿٤﴾

Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika.[475]

وَتَكُونُ ٱلْجِبَالُ كَٱلْعِهْنِ ٱلْمَنفُوشِ ﴿٥﴾

Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga).

فَأَمَّا مَن ثَقُلَتْ مَوَٰزِينُهُۥ ﴿٦﴾

Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa).[476]

فَهُوَ فِى عِيشَةٍۢ رَّاضِيَةٍۢ ﴿٧﴾

Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro).

وَأَمَّا مَنْ خَفَّتْ مَوَٰزِينُهُۥ ﴿٨﴾

Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa),

فَأُمُّهُۥ هَاوِيَةٌۭ ﴿٩﴾

Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya.

وَمَآ أَدْرَىٰكَ مَا هِيَهْ ﴿١٠﴾

Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya?

نَارٌ حَامِيَةٌۢ ﴿١١﴾

Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali!