Main pages

Surah Ash-Shuara ( The Poets )

Chewa

Surah Ash-Shuara ( The Poets ) - Aya count 227

طسٓمٓ ﴿١﴾

Tâ-Sîn-Mîm.

تِلْكَ ءَايَٰتُ ٱلْكِتَٰبِ ٱلْمُبِينِ ﴿٢﴾

Izi ndi Ayah (ndime) za buku (la Qur’an) lofotokoza chilichonse (chofunika m’chipembedzo).

لَعَلَّكَ بَٰخِعٌۭ نَّفْسَكَ أَلَّا يَكُونُواْ مُؤْمِنِينَ ﴿٣﴾

Mwina iwe (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) udziononga wekha (ndi madandaulo) chifukwa chakuti (iwo) sadakhale okhulupirira.

إِن نَّشَأْ نُنَزِّلْ عَلَيْهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ ءَايَةًۭ فَظَلَّتْ أَعْنَٰقُهُمْ لَهَا خَٰضِعِينَ ﴿٤﴾

Tikadafuna, tikadawatsitsira chizizwa kuchokera kumwamba; kotero kuti makosi awo akadadzichepetsa ndi chizizwacho, (sakadatha kucheukira kwina koma sitifuna kukakamiza anthu kuti akhale Asilamu).[295]

وَمَا يَأْتِيهِم مِّن ذِكْرٍۢ مِّنَ ٱلرَّحْمَٰنِ مُحْدَثٍ إِلَّا كَانُواْ عَنْهُ مُعْرِضِينَ ﴿٥﴾

Ndipo palibe pamene chikuwadzera chivumbulutso chatsopano chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri koma amazipatula ku icho (chivumbulutso).

فَقَدْ كَذَّبُواْ فَسَيَأْتِيهِمْ أَنۢبَٰٓؤُاْ مَا كَانُواْ بِهِۦ يَسْتَهْزِءُونَ ﴿٦﴾

Ndithu atsutsa; choncho posachedwapa ziwadzera nkhani zomwe adali kuzichitira chipongwe.

أَوَلَمْ يَرَوْاْ إِلَى ٱلْأَرْضِ كَمْ أَنۢبَتْنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوْجٍۢ كَرِيمٍ ﴿٧﴾

Kodi sadaone nthaka? Ndimmera ungati taumeretsa m’menemo kuchokera mu mtundu ulionse, wokongola?

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿٨﴾

Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro (zosonyeza mphamvu za Allah). Koma ambiri a iwo sali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿٩﴾

Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.

وَإِذْ نَادَىٰ رَبُّكَ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱئْتِ ٱلْقَوْمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴿١٠﴾

Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako adaitana (m’neneri) Mûsa; adamuuza: “Pita kwa anthu ochita zoipa.”

قَوْمَ فِرْعَوْنَ ۚ أَلَا يَتَّقُونَ ﴿١١﴾

Anthu a Farawo; (auze): “Kodi sawopa (Allah)?”

قَالَ رَبِّ إِنِّىٓ أَخَافُ أَن يُكَذِّبُونِ ﴿١٢﴾

(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ine ndikuopa kuti anganditsutse.

وَيَضِيقُ صَدْرِى وَلَا يَنطَلِقُ لِسَانِى فَأَرْسِلْ إِلَىٰ هَٰرُونَ ﴿١٣﴾

Ndipo chingabanike chifuwa changa (ndi maganizo, chifukwa chakunditsutsa kwawo); ndiponso lirime langa siliyankhula momveka bwino. Choncho tumizaninso uthengawu kwa Harun (kuti tikhale awiri ndipo azikandithangata pantchito yangayi).

وَلَهُمْ عَلَىَّ ذَنۢبٌۭ فَأَخَافُ أَن يَقْتُلُونِ ﴿١٤﴾

Ndipo iwowo ndili nawo mlandu ndipo ndikuopa kuti angandiphe (pobwezera chimene ndidawalakwira powaphera munthu wawo).

قَالَ كَلَّا ۖ فَٱذْهَبَا بِـَٔايَٰتِنَآ ۖ إِنَّا مَعَكُم مُّسْتَمِعُونَ ﴿١٥﴾

(Allah) adati: “Iyayi! Pitani pamodzi ndi zozizwa Zathu; ndithu Ife tikakhala nanu limodzi (pokuthangatani) uku tikumvetsera (zimene azikanena).”

فَأْتِيَا فِرْعَوْنَ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولُ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٦﴾

“Choncho mpitireni Farawo, ndipo kamuuzeni kuti: “Ife ndi atumiki a Mbuye wa zolengedwa zonse.”

أَنْ أَرْسِلْ مَعَنَا بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ ﴿١٧﴾

“(Tatumidwa) kuti uwapereke kwa ife ana a Israyeli (kuti tinke nawo ku Sham).”

قَالَ أَلَمْ نُرَبِّكَ فِينَا وَلِيدًۭا وَلَبِثْتَ فِينَا مِنْ عُمُرِكَ سِنِينَ ﴿١٨﴾

(Farawo) adati (kwa Mûsa): “Kodi sitidakulere kwathu uli mwana, ndi kukhala nafe pa moyo wako zaka zambiri?”

وَفَعَلْتَ فَعْلَتَكَ ٱلَّتِى فَعَلْتَ وَأَنتَ مِنَ ٱلْكَٰفِرِينَ ﴿١٩﴾

“Ndipo udachita chochita chako chimene udachichita, ndipo iwe ndiwe mmodzi wa osathokoza!”

قَالَ فَعَلْتُهَآ إِذًۭا وَأَنَا۠ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ ﴿٢٠﴾

(Mûsa) adati: “Ndidachita zimenezo pomwe ine ndidali mmodzi wa osazindikira zinthu.”

فَفَرَرْتُ مِنكُمْ لَمَّا خِفْتُكُمْ فَوَهَبَ لِى رَبِّى حُكْمًۭا وَجَعَلَنِى مِنَ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿٢١﴾

“Choncho ndidakuthawani pomwe ndidakuopani; tsono Mbuye wanga wandipatsa nzeru zoweruzira (zinthu), ndi kundisankha kukhala mmodzi wa atumiki.”

وَتِلْكَ نِعْمَةٌۭ تَمُنُّهَا عَلَىَّ أَنْ عَبَّدتَّ بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ ﴿٢٢﴾

“Ndipo kodi umenewu ndimtendere wonditonzera pomwe mudawaika muukapolo ana a Israyeli!”

قَالَ فِرْعَوْنُ وَمَا رَبُّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿٢٣﴾

Farawo adati: “Kodi ndani Mbuye wa zolengedwayo?”

قَالَ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَآ ۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ ﴿٢٤﴾

(Mûsa) adati: “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo. (Amachita chilichonse m’menemo mmene wafunira; kupereka moyo ndi imfa).”

قَالَ لِمَنْ حَوْلَهُۥٓ أَلَا تَسْتَمِعُونَ ﴿٢٥﴾

(Farawo) adauza omwe adali m’mphepete mwake (mwachipongwe): “Kodi simukumva (mawu achibwanawa)?”

قَالَ رَبُّكُمْ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿٢٦﴾

(Mûsa adapitiriza kunena) adati: “Allah ndi Mbuye wanu komanso Mbuye wamakolo anu oyamba.”

قَالَ إِنَّ رَسُولَكُمُ ٱلَّذِىٓ أُرْسِلَ إِلَيْكُمْ لَمَجْنُونٌۭ ﴿٢٧﴾

(Farawo) adati (kwa anthu ake pofuna kuwakwiitsa): “Ndithu Mtumiki wanu amene watumidwa kwa inu, ngwamisala.”

قَالَ رَبُّ ٱلْمَشْرِقِ وَٱلْمَغْرِبِ وَمَا بَيْنَهُمَآ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْقِلُونَ ﴿٢٨﴾

(Mûsa) adati: “Mbuye wakuvuma ndi kuzambwe, ndi zomwe ziri pakati pake ngati mumazindikira (zinthu, muzindikira izi).”

قَالَ لَئِنِ ٱتَّخَذْتَ إِلَٰهًا غَيْرِى لَأَجْعَلَنَّكَ مِنَ ٱلْمَسْجُونِينَ ﴿٢٩﴾

(Farawo) adati: “Ngati udzipangira mulungu wina kusiya ine, ndikuchita kukhala mmodzi wa omangidwa kundende.”

قَالَ أَوَلَوْ جِئْتُكَ بِشَىْءٍۢ مُّبِينٍۢ ﴿٣٠﴾

(Mûsa) adati: “Kodi ngakhale nditakubweretsera chinthu choonekera poyera (chosonyeza kuti zimene ndikunenazi ndizoona ndatumidwa ndi Allah)?”

قَالَ فَأْتِ بِهِۦٓ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ﴿٣١﴾

(Farawo) adati: “Chibweretse, ngati uli mwa onena zoona.”

فَأَلْقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِىَ ثُعْبَانٌۭ مُّبِينٌۭ ﴿٣٢﴾

Ndipo (Mûsa) adaponya (pansi) ndodo yake, mwadzidzidzi idasanduka njoka yopenyeka.

وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِىَ بَيْضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ ﴿٣٣﴾

Ndipo adatulutsa dzanja lake; pompo lidali loyera (kwambiri) kwa (onse) openya.

قَالَ لِلْمَلَإِ حَوْلَهُۥٓ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمٌۭ ﴿٣٤﴾

(Farawo) adauza akuluakulu omwe adali m’mphepete mwake: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa kwambiri.”

يُرِيدُ أَن يُخْرِجَكُم مِّنْ أَرْضِكُم بِسِحْرِهِۦ فَمَاذَا تَأْمُرُونَ ﴿٣٥﴾

“Akufuna kukutulutsani m’dziko lanu ndi matsenga ake; kodi nanga mukuti chiyani?”[296]

قَالُوٓاْ أَرْجِهْ وَأَخَاهُ وَٱبْعَثْ فِى ٱلْمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ ﴿٣٦﴾

(Anthu) adati (kwa Farawo): “Mpatse nthawi ndi m’bale wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) m’mizinda yonse osonkhanitsa anthu.”

يَأْتُوكَ بِكُلِّ سَحَّارٍ عَلِيمٍۢ ﴿٣٧﴾

“Ndipo akubweretsera amatsenga onse odziwa kwabasi (kotero kuti adzampambana Mûsa).”

فَجُمِعَ ٱلسَّحَرَةُ لِمِيقَٰتِ يَوْمٍۢ مَّعْلُومٍۢ ﴿٣٨﴾

Choncho amatsenga adasonkhanitsidwa mu nthawi ya tsiku lodziwika.

وَقِيلَ لِلنَّاسِ هَلْ أَنتُم مُّجْتَمِعُونَ ﴿٣٩﴾

Ndipo anthu adauzidwa: “Kodi inu musonkhana? (Choncho, sonkhanani).”

لَعَلَّنَا نَتَّبِعُ ٱلسَّحَرَةَ إِن كَانُواْ هُمُ ٱلْغَٰلِبِينَ ﴿٤٠﴾

“Mwina tingawatsatire amatsenga ngati iwo ndiamene apambane.”

فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالُواْ لِفِرْعَوْنَ أَئِنَّ لَنَا لَأَجْرًا إِن كُنَّا نَحْنُ ٱلْغَٰلِبِينَ ﴿٤١﴾

Ndipo pamene amatsenga adadza, adati kwa Farawo: “Kodi tidzakhala ndi mphoto ngati ife ndife tipambane?”

قَالَ نَعَمْ وَإِنَّكُمْ إِذًۭا لَّمِنَ ٱلْمُقَرَّبِينَ ﴿٤٢﴾

(Farawo) adati: “Inde, (ndipo kuonjezera apo) ndithu inu mudzakhala mwa amene amakhala pafupi (ndi ine, monga nduna zanga).”

قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلْقُواْ مَآ أَنتُم مُّلْقُونَ ﴿٤٣﴾

Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zimene mufuna kuponya (zosonyeza kuya kwa matsenga anu).”

فَأَلْقَوْاْ حِبَالَهُمْ وَعِصِيَّهُمْ وَقَالُواْ بِعِزَّةِ فِرْعَوْنَ إِنَّا لَنَحْنُ ٱلْغَٰلِبُونَ ﴿٤٤﴾

Choncho adaponya zingwe zawo ndi ndodo zawo, ndipo adati: “Kupyolera mu mphamvu za Farawo, ndithu ife ndife opambana.”

فَأَلْقَىٰ مُوسَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِىَ تَلْقَفُ مَا يَأْفِكُونَ ﴿٤٥﴾

Kenako Mûsa adaponya ndodo yake; mwadzidzidzi iyo idameza zabodza zomwe iwo adakonza.

فَأُلْقِىَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ ﴿٤٦﴾

Pamenepo amatsenga adadzigwetsa pansi molambira.

قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿٤٧﴾

Adati: “Tamkhulupirira Mbuye wa zolengedwa.”

رَبِّ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ﴿٤٨﴾

“Mbuye wa Mûsa ndi Harun.”

قَالَ ءَامَنتُمْ لَهُۥ قَبْلَ أَنْ ءَاذَنَ لَكُمْ ۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِى عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحْرَ فَلَسَوْفَ تَعْلَمُونَ ۚ لَأُقَطِّعَنَّ أَيْدِيَكُمْ وَأَرْجُلَكُم مِّنْ خِلَٰفٍۢ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمْ أَجْمَعِينَ ﴿٤٩﴾

(Farawo) adati: “Ha! Mwamkhulupirira chotani ndisanakulolezeni? Ndithu iyeyu ndimkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Choncho posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni) ndithu ndidula manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa (podula mkono wakumanja ndi mwendo wakumanzere; kapena kudula mkono wakumanzere ndi mwendo wakumanja), ndipo kenako ndikupachikani nonsenu.”

قَالُواْ لَا ضَيْرَ ۖ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ ﴿٥٠﴾

(Amatsenga) adati: “Palibe vuto, ndithu ife (tonse) tibwerera kwa Mbuye wathu.”

إِنَّا نَطْمَعُ أَن يَغْفِرَ لَنَا رَبُّنَا خَطَٰيَٰنَآ أَن كُنَّآ أَوَّلَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿٥١﴾

“Ndithu ife tikuyembekezera kuti Mbuye wathu atikhululukire zolakwa zathu; pokhala oyamba mwa okhulupirira.”

۞ وَأَوْحَيْنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنْ أَسْرِ بِعِبَادِىٓ إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ ﴿٥٢﴾

Ndipo tidamvumbulutsira Mûsa (kuti): “Pita ndi anthu anga m’nthawi yausiku (musamuke m’dziko la Iguputo); ndithu inu mutsatidwa.”

فَأَرْسَلَ فِرْعَوْنُ فِى ٱلْمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ ﴿٥٣﴾

Choncho Farawo adatuma (owatuma) kuti asonkhanitse anthu m’mizinda (kuti aletse ana a Israyeli kutuluka).

إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَشِرْذِمَةٌۭ قَلِيلُونَ ﴿٥٤﴾

(Adawauza otumidwa aja kuti auze anthu kuti): “Ndithu awa (ana a Israyeli) ndikagulu kochepa.

وَإِنَّهُمْ لَنَا لَغَآئِظُونَ ﴿٥٥﴾

Ndipo ndithu iwo akutikwiitsa.

وَإِنَّا لَجَمِيعٌ حَٰذِرُونَ ﴿٥٦﴾

Koma ndithu ife tonse (ndife ochuluka komabe ngakhale zili choncho) tikuwaopa.”

فَأَخْرَجْنَٰهُم مِّن جَنَّٰتٍۢ وَعُيُونٍۢ ﴿٥٧﴾

Choncho tidawatulutsa m’minda ndi mwa akasupe.

وَكُنُوزٍۢ وَمَقَامٍۢ كَرِيمٍۢ ﴿٥٨﴾

Ndi m’nkhokwe za chuma ndi m’malo okongola.

كَذَٰلِكَ وَأَوْرَثْنَٰهَا بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ ﴿٥٩﴾

Momwemo ndi mmene tidawachitira ndipo tidawalowetsera chokolo zinthu zawo zonse kwa ana a Israyeli.

فَأَتْبَعُوهُم مُّشْرِقِينَ ﴿٦٠﴾

Choncho (anthu a Farawo ndi iye mwini) adawatsatira (ana a Israyeli) dzuwa litatuluka.

فَلَمَّا تَرَٰٓءَا ٱلْجَمْعَانِ قَالَ أَصْحَٰبُ مُوسَىٰٓ إِنَّا لَمُدْرَكُونَ ﴿٦١﴾

Ndipo pamene magulu awiri adaonana (anthu a Farawo ndi anthu a Mûsa), anthu a Mûsa adati: “Ndithu ife tigwidwa.”

قَالَ كَلَّآ ۖ إِنَّ مَعِىَ رَبِّى سَيَهْدِينِ ﴿٦٢﴾

(Mûsa) adati: “Iyayi! Ndithu Mbuye wanga ali nane pamodzi. Andiongolera (kuti ife tonse tipulumuke).”

فَأَوْحَيْنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱضْرِب بِّعَصَاكَ ٱلْبَحْرَ ۖ فَٱنفَلَقَ فَكَانَ كُلُّ فِرْقٍۢ كَٱلطَّوْدِ ٱلْعَظِيمِ ﴿٦٣﴾

Ndipo tidam’vumbulutsira mawu Mûsa (akuti): “Menya nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo idagawikana, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu.

وَأَزْلَفْنَا ثَمَّ ٱلْءَاخَرِينَ ﴿٦٤﴾

Ndipo tidawayandikitsa pamenepo anthu enawo, (Farawo ndi anthu ake nalowa pa njira yomweyo pambuyo pa Mûsa ndi anthu ake).

وَأَنجَيْنَا مُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓ أَجْمَعِينَ ﴿٦٥﴾

Ndipo tidapulumutsa Mûsa ndi onse amene adali nawo (mpaka adaoloka nyanjayo, madzi ali chiimire mbali iyi ndi iyi).

ثُمَّ أَغْرَقْنَا ٱلْءَاخَرِينَ ﴿٦٦﴾

Kenako tidawamiza enawo, (Farawo ndi anthu ake).

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿٦٧﴾

Ndithu pa zimenezi pali lingaliro. Koma ambiri a iwo sali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿٦٨﴾

Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa (amalanga ndi chilango choopsa omwe amunyoza); Wachisoni (kwa omkhulupirira ndi kumumvera).

وَٱتْلُ عَلَيْهِمْ نَبَأَ إِبْرَٰهِيمَ ﴿٦٩﴾

Ndipo awerengere (osakhulupirira) nkhani ya (M’neneri) Ibrahim.

إِذْ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوْمِهِۦ مَا تَعْبُدُونَ ﴿٧٠﴾

Pamene adafunsa bambo wake ndi anthu ake (kuti); “Kodi mukupembedza chiyani?”

قَالُواْ نَعْبُدُ أَصْنَامًۭا فَنَظَلُّ لَهَا عَٰكِفِينَ ﴿٧١﴾

Adati: “Tikupembedza mafano; ndipo tipitiriza kuwapembedza.”

قَالَ هَلْ يَسْمَعُونَكُمْ إِذْ تَدْعُونَ ﴿٧٢﴾

(Ibrahim) adati: “Kodi amakumvani mukawaitana?”

أَوْ يَنفَعُونَكُمْ أَوْ يَضُرُّونَ ﴿٧٣﴾

“Kapena amakuthandizani (mukawapembedza) kapena amapereka masautso kwa inu (mukasiya kuwapembedza)?”

قَالُواْ بَلْ وَجَدْنَآ ءَابَآءَنَا كَذَٰلِكَ يَفْعَلُونَ ﴿٧٤﴾

(Iwo) adati: “Koma tidapeza makolo athu akuchita zimenezi.”

قَالَ أَفَرَءَيْتُم مَّا كُنتُمْ تَعْبُدُونَ ﴿٧٥﴾

(Ibrahim) adati: “Kodi mukuwaona awa amene mwakhala mukuwapembedza,”

أَنتُمْ وَءَابَآؤُكُمُ ٱلْأَقْدَمُونَ ﴿٧٦﴾

“Inu ndi makolo anu amene adatsogola?”

فَإِنَّهُمْ عَدُوٌّۭ لِّىٓ إِلَّا رَبَّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿٧٧﴾

“Ndithu iwo ndiadani anga, kupatula Mbuye wa zolengedwa zonse;”

ٱلَّذِى خَلَقَنِى فَهُوَ يَهْدِينِ ﴿٧٨﴾

“Yemwe adandilenga, ndiponso Yemwe akundiongolera (kunjira yolungama);”

وَٱلَّذِى هُوَ يُطْعِمُنِى وَيَسْقِينِ ﴿٧٩﴾

“Ndiyemwe akundidyetsa ndi kundimwetsa.”

وَإِذَا مَرِضْتُ فَهُوَ يَشْفِينِ ﴿٨٠﴾

“Ndipo ndikadwala ndiyemwe amandichiritsa.”

وَٱلَّذِى يُمِيتُنِى ثُمَّ يُحْيِينِ ﴿٨١﴾

“Ndi Amene adzandipatsa imfa, ndipo (tsiku la Qiyâma) adzandidzutsa;”

وَٱلَّذِىٓ أَطْمَعُ أَن يَغْفِرَ لِى خَطِيٓـَٔتِى يَوْمَ ٱلدِّينِ ﴿٨٢﴾

“Ndi Yemwe ndikuyembekezera kuti adzandikhululukira zolakwa zanga tsiku la malipiro.”

رَبِّ هَبْ لِى حُكْمًۭا وَأَلْحِقْنِى بِٱلصَّٰلِحِينَ ﴿٨٣﴾

“E Mbuye wanga! Ndipatseni nzeru zoweruzira (zinthu), ndikundilumikiza ndi anthu abwino;”

وَٱجْعَل لِّى لِسَانَ صِدْقٍۢ فِى ٱلْءَاخِرِينَ ﴿٨٤﴾

“Ndipatseni kutchulidwa kwabwino kwa anthu ena odza pambuyo;”

وَٱجْعَلْنِى مِن وَرَثَةِ جَنَّةِ ٱلنَّعِيمِ ﴿٨٥﴾

“Ndichiteni kukhala mmodzi mwa olandira Munda wamtendere;”

وَٱغْفِرْ لِأَبِىٓ إِنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ ﴿٨٦﴾

“Ndipo khululukirani bambo wanga; ndithu iye adali mmodzi wa osokera;”

وَلَا تُخْزِنِى يَوْمَ يُبْعَثُونَ ﴿٨٧﴾

“Ndipo musadzandiyalutse pa tsiku loukitsidwa anthu (ku imfa);”

يَوْمَ لَا يَنفَعُ مَالٌۭ وَلَا بَنُونَ ﴿٨٨﴾

“Tsiku lomwe chuma ndi ana sizidzathandiza (aliyense).”

إِلَّا مَنْ أَتَى ٱللَّهَ بِقَلْبٍۢ سَلِيمٍۢ ﴿٨٩﴾

“Kupatula yemwe adzadza kwa Allah ndi mtima woyera (iye ndiamene adzathandizidwa patsikulo).”

وَأُزْلِفَتِ ٱلْجَنَّةُ لِلْمُتَّقِينَ ﴿٩٠﴾

Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa kwa oopa (Allah),

وَبُرِّزَتِ ٱلْجَحِيمُ لِلْغَاوِينَ ﴿٩١﴾

Ndipo Jahannam idzaonetsedwa kwa opotoka;

وَقِيلَ لَهُمْ أَيْنَ مَا كُنتُمْ تَعْبُدُونَ ﴿٩٢﴾

Ndipo kudzanenedwa kwa iwo: “Ali kuti amene mudali kuwapembedza aja,

مِن دُونِ ٱللَّهِ هَلْ يَنصُرُونَكُمْ أَوْ يَنتَصِرُونَ ﴿٩٣﴾

M’malo mwa Allah? Kodi angathe kukuthandizani kapena kudzithandiza okha?”

فَكُبْكِبُواْ فِيهَا هُمْ وَٱلْغَاوُۥنَ ﴿٩٤﴾

Ndipo iwo ndi opotoka ena adzaponyedwa ndi nkhope zawo m’menemo (mu Jahannam).

وَجُنُودُ إِبْلِيسَ أَجْمَعُونَ ﴿٩٥﴾

Ndi magulu onse ankhondo a Iblis (omwe adali kukometsa kwa anthu zoipa ndi machimo).

قَالُواْ وَهُمْ فِيهَا يَخْتَصِمُونَ ﴿٩٦﴾

Adzanena (movomereza kulakwa kwawo) uku naonso ali m’menemo, akukangana (ndi anzawo omwe adawasokeretsa):

تَٱللَّهِ إِن كُنَّا لَفِى ضَلَٰلٍۢ مُّبِينٍ ﴿٩٧﴾

“Ndikulumbira Allah, ndithu tidali m’kusokera kowonekera.

إِذْ نُسَوِّيكُم بِرَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿٩٨﴾

Pamene timakufananitsani ndi Mbuye wa zolengedwa.

وَمَآ أَضَلَّنَآ إِلَّا ٱلْمُجْرِمُونَ ﴿٩٩﴾

Ndipo sadatisokeretse, koma oipa okha basi.

فَمَا لَنَا مِن شَٰفِعِينَ ﴿١٠٠﴾

Choncho ife tilibe aomboli (otiombola),

وَلَا صَدِيقٍ حَمِيمٍۢ ﴿١٠١﴾

Ngakhalenso bwenzi wapamtima (woti angatipulumutse kumasautsowa).

فَلَوْ أَنَّ لَنَا كَرَّةًۭ فَنَكُونَ مِنَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿١٠٢﴾

Tikadapeza mwayi wobwerera (ku moyo wa padziko), tikadakhala mwa okhulupirira.”

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٠٣﴾

Ndithu m’zimenezi, muli malingaliro akulu, koma ambiri a iwo sali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٠٤﴾

Ndipo ndithu Mbuye wako, ndiye Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.

كَذَّبَتْ قَوْمُ نُوحٍ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿١٠٥﴾

Anthu a Nuh adatsutsa atumiki.

إِذْ قَالَ لَهُمْ أَخُوهُمْ نُوحٌ أَلَا تَتَّقُونَ ﴿١٠٦﴾

Pamene adawauza Nuh m’bale wawo kuti: “Kodi simukuopa (Allah ngakhale nditakuuzani zoopsa zimene zikukudikirani)?”

إِنِّى لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌۭ ﴿١٠٧﴾

“Ndithu ine kwa inu ndine Mtumiki wokhulupirika;”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٠٨﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

وَمَآ أَسْـَٔلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِىَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٠٩﴾

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١١٠﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

۞ قَالُوٓاْ أَنُؤْمِنُ لَكَ وَٱتَّبَعَكَ ٱلْأَرْذَلُونَ ﴿١١١﴾

(Iwo) adati: “Nchotani kuti tikukhulupirire iwe chikhalirecho anthu wamba ndi amene akukutsatira?”

قَالَ وَمَا عِلْمِى بِمَا كَانُواْ يَعْمَلُونَ ﴿١١٢﴾

(Nuh) adati: “Sindikudziwa zimene adali kuchita (zomwe zachititsa kuti Allah awaongolere kunjira yoongoka).”

إِنْ حِسَابُهُمْ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّى ۖ لَوْ تَشْعُرُونَ ﴿١١٣﴾

“Chiwerengero chawo sichili kwina koma kwa Mbuye wanga, mukadakhala mukuzindikira.”

وَمَآ أَنَا۠ بِطَارِدِ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿١١٤﴾

“Ndipo sindine wopirikitsa okhulupirira (ku chipembedzo cha Allah kuti inu olemekezeka muchikhulupirire).”

إِنْ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرٌۭ مُّبِينٌۭ ﴿١١٥﴾

“Ine sikanthu , koma ndine mchenjezi woonekera.”

قَالُواْ لَئِن لَّمْ تَنتَهِ يَٰنُوحُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلْمَرْجُومِينَ ﴿١١٦﴾

(Iwo) adati: “Ngati susiya, iwe Nuh, (zonena zakozi) ndithu ukhala mmodzi mwa ogendedwa (miyala mpaka ufe).”

قَالَ رَبِّ إِنَّ قَوْمِى كَذَّبُونِ ﴿١١٧﴾

(Nuh) adati (kwa Allah): “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga anditsutsa.”

فَٱفْتَحْ بَيْنِى وَبَيْنَهُمْ فَتْحًۭا وَنَجِّنِى وَمَن مَّعِىَ مِنَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿١١٨﴾

Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pa iwo (chiweruzo chabwino), ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupirira.”

فَأَنجَيْنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِى ٱلْفُلْكِ ٱلْمَشْحُونِ ﴿١١٩﴾

Choncho, tidampulumutsa pamodzi ndi omwe adali naye m’chombo chodzadza (ndi chilichonse chamoyo chomwe chidalipo m’dziko, chachimuna ndi chachikazi chidaikidwa m’menemo).

ثُمَّ أَغْرَقْنَا بَعْدُ ٱلْبَاقِينَ ﴿١٢٠﴾

Pambuyo pake tidawamiza otsalawo.

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٢١﴾

Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٢٢﴾

Ndipo ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha.

كَذَّبَتْ عَادٌ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿١٢٣﴾

Naonso Âdi adatsutsa atumiki.

إِذْ قَالَ لَهُمْ أَخُوهُمْ هُودٌ أَلَا تَتَّقُونَ ﴿١٢٤﴾

Pamene m’bale wawo (Mneneri) Hûd adawafunsa kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”

إِنِّى لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌۭ ﴿١٢٥﴾

“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu;”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٢٦﴾

“Choncho, muopeni Allah ndipo mverani ine.”

وَمَآ أَسْـَٔلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِىَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٢٧﴾

“Ndipo pazimenezi sindikukupemphani malipiro; ndithu malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

أَتَبْنُونَ بِكُلِّ رِيعٍ ءَايَةًۭ تَعْبَثُونَ ﴿١٢٨﴾

“Kodi mukudzimangira nyumba pamalo paliponse pachitunda pokongola, moseweretsa?”

وَتَتَّخِذُونَ مَصَانِعَ لَعَلَّكُمْ تَخْلُدُونَ ﴿١٢٩﴾

“Ndipo mukudzimangira (nyumba zonga) linga ngati kuti mukuona kuti mudzakhala muyaya?”

وَإِذَا بَطَشْتُم بَطَشْتُمْ جَبَّارِينَ ﴿١٣٠﴾

“Ndipo mukamamenya nkhondo mumamenya modzitukumula.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٣١﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِىٓ أَمَدَّكُم بِمَا تَعْلَمُونَ ﴿١٣٢﴾

“Ndipo muopeni Yemwe adakupatsani zimene mukuzidziwa.”

أَمَدَّكُم بِأَنْعَٰمٍۢ وَبَنِينَ ﴿١٣٣﴾

“Adakupatsani ziweto ndi ana.”

وَجَنَّٰتٍۢ وَعُيُونٍ ﴿١٣٤﴾

“Ndi minda ndi akasupe.”

إِنِّىٓ أَخَافُ عَلَيْكُمْ عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍۢ ﴿١٣٥﴾

“Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”

قَالُواْ سَوَآءٌ عَلَيْنَآ أَوَعَظْتَ أَمْ لَمْ تَكُن مِّنَ ٱلْوَٰعِظِينَ ﴿١٣٦﴾

Iwo adati: “Kwa ife nchimodzimodzi, utichenjeze kapena iwe usakhale mmodzi mwa ochenjeza.”

إِنْ هَٰذَآ إِلَّا خُلُقُ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿١٣٧﴾

“Ndithu kutero (anthu ena kudzitcha atumiki a Allah), sikanthu koma ndi machitidwe a anthu akale.”

وَمَا نَحْنُ بِمُعَذَّبِينَ ﴿١٣٨﴾

“Ndipo ife sitidzalangidwa (monga momwe ukunenera).”

فَكَذَّبُوهُ فَأَهْلَكْنَٰهُمْ ۗ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٣٩﴾

Choncho adamtsutsa, ndipo tidawaononga. Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٤٠﴾

Ndipo ndithu Mbuye wako ndiye Wamphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.

كَذَّبَتْ ثَمُودُ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿١٤١﴾

A Samudu (naonso) adatsutsa atumiki.

إِذْ قَالَ لَهُمْ أَخُوهُمْ صَٰلِحٌ أَلَا تَتَّقُونَ ﴿١٤٢﴾

Pamene m’bale wawo Swalih adawauza kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”

إِنِّى لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌۭ ﴿١٤٣﴾

“Ndithu ine ndimtumiki wokhulupirika kwa inu.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٤٤﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo mverani ine.”

وَمَآ أَسْـَٔلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِىَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٤٥﴾

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi. Palibe kumene kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wa zolengedwa.”

أَتُتْرَكُونَ فِى مَا هَٰهُنَآ ءَامِنِينَ ﴿١٤٦﴾

“Kodi (mukuganizira kuti) mudzasiidwa mwamtendere pa izi zili pano (popanda imfa kukudzerani?)”

فِى جَنَّٰتٍۢ وَعُيُونٍۢ ﴿١٤٧﴾

“M’minda ndi mu akasupe?”

وَزُرُوعٍۢ وَنَخْلٍۢ طَلْعُهَا هَضِيمٌۭ ﴿١٤٨﴾

“Ndi (m’minda) yammera ndi mitengo yakanjedza yamikoko yakupsa yofewa?”

وَتَنْحِتُونَ مِنَ ٱلْجِبَالِ بُيُوتًۭا فَٰرِهِينَ ﴿١٤٩﴾

“Ndipo mukugoba nyumba m’mapiri mwaluso.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٥٠﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

وَلَا تُطِيعُوٓاْ أَمْرَ ٱلْمُسْرِفِينَ ﴿١٥١﴾

“Ndipo musamvere za awo opyola malire.”

ٱلَّذِينَ يُفْسِدُونَ فِى ٱلْأَرْضِ وَلَا يُصْلِحُونَ ﴿١٥٢﴾

“Amene akuononga pa dziko, ndipo sakonza.”

قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلْمُسَحَّرِينَ ﴿١٥٣﴾

Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”

مَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٌۭ مِّثْلُنَا فَأْتِ بِـَٔايَةٍ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ﴿١٥٤﴾

“Iwe suli kanthu, koma munthu ngati ife; tabwera ndi chozizwitsa, ngati ndiwedi mmodzi wa onena zoona!”

قَالَ هَٰذِهِۦ نَاقَةٌۭ لَّهَا شِرْبٌۭ وَلَكُمْ شِرْبُ يَوْمٍۢ مَّعْلُومٍۢ ﴿١٥٥﴾

Iye adati: “(Ndakubweretserani) ngamira iyi yaikazi; (koma) ili ndi gawo lake lakumwa, ndipo inu muli ndi gawo lanu lakutunga (madzi) patsiku lodziwika. (Tsiku lina lotunga rnadzi anthu).”

وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٍۢ فَيَأْخُذَكُمْ عَذَابُ يَوْمٍ عَظِيمٍۢ ﴿١٥٦﴾

“Ndipo musaikhudze ndi choipa chilichonse kuopera kuti chingakupezeni chilango cha tsiku lalikulu.”

فَعَقَرُوهَا فَأَصْبَحُواْ نَٰدِمِينَ ﴿١٥٧﴾

Koma iwo adaipha; ndipo adali odzinena (pamene chidadza chilango cha Allah).

فَأَخَذَهُمُ ٱلْعَذَابُ ۗ إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٥٨﴾

Choncho chilango (cha Allah) chidawaononga, ndithu pa zimenezi pali phunziro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٥٩﴾

Ndipo, ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; wachisoni chosatha.

كَذَّبَتْ قَوْمُ لُوطٍ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿١٦٠﴾

Anthu a Luti adatsutsa atumiki.

إِذْ قَالَ لَهُمْ أَخُوهُمْ لُوطٌ أَلَا تَتَّقُونَ ﴿١٦١﴾

Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?”

إِنِّى لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌۭ ﴿١٦٢﴾

“Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٦٣﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

وَمَآ أَسْـَٔلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِىَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٦٤﴾

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; palibe komwe kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wazolengedwa.”

أَتَأْتُونَ ٱلذُّكْرَانَ مِنَ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٦٥﴾

“Kodi mukugonana ndi amuna (anzanu) muzolengedwa (za Allah),

وَتَذَرُونَ مَا خَلَقَ لَكُمْ رَبُّكُم مِّنْ أَزْوَٰجِكُم ۚ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ عَادُونَ ﴿١٦٦﴾

“Ndikusiya amene Mbuye wanu adakulengerani kuti akhale akazi anu? Ndithu inu ndinu anthu olumpha malire.”

قَالُواْ لَئِن لَّمْ تَنتَهِ يَٰلُوطُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلْمُخْرَجِينَ ﴿١٦٧﴾

Iwo adati: “Ngati susiya (izi), E iwe Luti! ndithu ukhala mmodzi wa opirikitsidwa.”

قَالَ إِنِّى لِعَمَلِكُم مِّنَ ٱلْقَالِينَ ﴿١٦٨﴾

Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).”

رَبِّ نَجِّنِى وَأَهْلِى مِمَّا يَعْمَلُونَ ﴿١٦٩﴾

“E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.”

فَنَجَّيْنَٰهُ وَأَهْلَهُۥٓ أَجْمَعِينَ ﴿١٧٠﴾

Ndipo tidampulumutsa iye ndi onse a pa banja lake,

إِلَّا عَجُوزًۭا فِى ٱلْغَٰبِرِينَ ﴿١٧١﴾

Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo.

ثُمَّ دَمَّرْنَا ٱلْءَاخَرِينَ ﴿١٧٢﴾

Titatero tidawaononga enawo.

وَأَمْطَرْنَا عَلَيْهِم مَّطَرًۭا ۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلْمُنذَرِينَ ﴿١٧٣﴾

Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji, mvula ya ochenjezedwa!

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٧٤﴾

Ndithu pazimenezi pali malingaliro. Koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٧٥﴾

Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.

كَذَّبَ أَصْحَٰبُ لْـَٔيْكَةِ ٱلْمُرْسَلِينَ ﴿١٧٦﴾

Anthu a m’dziko lamitengo yambiri (Madiana) adatsutsa atumiki.

إِذْ قَالَ لَهُمْ شُعَيْبٌ أَلَا تَتَّقُونَ ﴿١٧٧﴾

(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?”

إِنِّى لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌۭ ﴿١٧٨﴾

“Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”

فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ﴿١٧٩﴾

“Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

وَمَآ أَسْـَٔلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ ۖ إِنْ أَجْرِىَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٨٠﴾

“Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; kulibe malipiro anga koma kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

۞ أَوْفُواْ ٱلْكَيْلَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلْمُخْسِرِينَ ﴿١٨١﴾

“Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).”

وَزِنُواْ بِٱلْقِسْطَاسِ ٱلْمُسْتَقِيمِ ﴿١٨٢﴾

“Ndipo yesani ndi sikelo yolungama (yolondola).”

وَلَا تَبْخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشْيَآءَهُمْ وَلَا تَعْثَوْاْ فِى ٱلْأَرْضِ مُفْسِدِينَ ﴿١٨٣﴾

“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo, ndiponso musayende padziko uku mukuononga.”

وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِى خَلَقَكُمْ وَٱلْجِبِلَّةَ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿١٨٤﴾

“Ndipo muopeni amene adalenga inu ndiponso zolengedwa zoyamba (zimene zidanka kale).”

قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلْمُسَحَّرِينَ ﴿١٨٥﴾

Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”

وَمَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٌۭ مِّثْلُنَا وَإِن نَّظُنُّكَ لَمِنَ ٱلْكَٰذِبِينَ ﴿١٨٦﴾

“Ndipo iwe suli kanthu koma munthu ngati ife, ndipo ndithu tikukutsimikizira kuti ndiwe mmodzi wa abodza.”

فَأَسْقِطْ عَلَيْنَا كِسَفًۭا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ﴿١٨٧﴾

“Choncho tigwetsere zidutswa za thambo (kuti zitiononge) ngati uli mmodzi wa onena zoona.”

قَالَ رَبِّىٓ أَعْلَمُ بِمَا تَعْمَلُونَ ﴿١٨٨﴾

(Shuaib) adati: “Mbuye wanga Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita. (Akadzaona kuti inu ngoyenera kulangidwa ndizidutswa za thambo, adzakulangani).”

فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَهُمْ عَذَابُ يَوْمِ ٱلظُّلَّةِ ۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍ ﴿١٨٩﴾

Koma adamutsutsa. Ndipo chidawagwera chilango chatsiku la mthunzi; ndithu chimenecho chidali chilango cha tsiku lalikulu.

إِنَّ فِى ذَٰلِكَ لَءَايَةًۭ ۖ وَمَا كَانَ أَكْثَرُهُم مُّؤْمِنِينَ ﴿١٩٠﴾

Ndithu pa zimenezi pali lingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira.

وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلْعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ﴿١٩١﴾

Ndipo, ndithu Mbuye wako Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha.

وَإِنَّهُۥ لَتَنزِيلُ رَبِّ ٱلْعَٰلَمِينَ ﴿١٩٢﴾

Ndipo, ndithu iyi (Qur’an) ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse.

نَزَلَ بِهِ ٱلرُّوحُ ٱلْأَمِينُ ﴿١٩٣﴾

Mzimu Wokhulupirika (Jiburil) udaivumbulutsa.

عَلَىٰ قَلْبِكَ لِتَكُونَ مِنَ ٱلْمُنذِرِينَ ﴿١٩٤﴾

Pa mtima wako kuti ukhale mmodzi wa achenjezi,

بِلِسَانٍ عَرَبِىٍّۢ مُّبِينٍۢ ﴿١٩٥﴾

M’chiyankhulo cha Chiarabu chomveka bwino.

وَإِنَّهُۥ لَفِى زُبُرِ ٱلْأَوَّلِينَ ﴿١٩٦﴾

Ndipo ndithu izi (zomwe zili m’Qur’an) zilipo m’mabuku akale.

أَوَلَمْ يَكُن لَّهُمْ ءَايَةً أَن يَعْلَمَهُۥ عُلَمَٰٓؤُاْ بَنِىٓ إِسْرَٰٓءِيلَ ﴿١٩٧﴾

Kodi sipadapezeke chisonyezo kwa iwo kuti akuidziwa (Qur’an) odziwa mwa ana a Israyeli (kotero kuti ena alowa m’Chisilamu)?

وَلَوْ نَزَّلْنَٰهُ عَلَىٰ بَعْضِ ٱلْأَعْجَمِينَ ﴿١٩٨﴾

Ndipo tikadaivumbulutsa kwa wina amene sali Muarabu,

فَقَرَأَهُۥ عَلَيْهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ مُؤْمِنِينَ ﴿١٩٩﴾

Kotero kuti nkuwawerengera momveka bwino, sakadaikhulupirira.

كَذَٰلِكَ سَلَكْنَٰهُ فِى قُلُوبِ ٱلْمُجْرِمِينَ ﴿٢٠٠﴾

Momwemo ndimo tidalowetsera kuitsutsa (Qur’an) m’mitima ya oipa.

لَا يُؤْمِنُونَ بِهِۦ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلْعَذَابَ ٱلْأَلِيمَ ﴿٢٠١﴾

Sangaikhulupirire kufikira ataona chilango chowawa.

فَيَأْتِيَهُم بَغْتَةًۭ وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ ﴿٢٠٢﴾

Choncho chidzawadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira.

فَيَقُولُواْ هَلْ نَحْنُ مُنظَرُونَ ﴿٢٠٣﴾

Tero adzayamba kunena: “Kodi ife tipatsidwa nthawi (yoti tilape)?”

أَفَبِعَذَابِنَا يَسْتَعْجِلُونَ ﴿٢٠٤﴾

Kodi akuchifulumizitsa chilango Chathu?

أَفَرَءَيْتَ إِن مَّتَّعْنَٰهُمْ سِنِينَ ﴿٢٠٥﴾

Kodi ukuona bwanji, ngati titawasangalatsa zaka (zankhaninkhani).

ثُمَّ جَآءَهُم مَّا كَانُواْ يُوعَدُونَ ﴿٢٠٦﴾

Kenako nkuwadzera (chilango) chomwe adalonjezedwa,

مَآ أَغْنَىٰ عَنْهُم مَّا كَانُواْ يُمَتَّعُونَ ﴿٢٠٧﴾

Sizidawathandize zomwe adali kusangalatsidwa nazozo.

وَمَآ أَهْلَكْنَا مِن قَرْيَةٍ إِلَّا لَهَا مُنذِرُونَ ﴿٢٠٨﴾

Ndipo sitidauononge mudzi uliwonse koma udali ndi achenjezi.

ذِكْرَىٰ وَمَا كُنَّا ظَٰلِمِينَ ﴿٢٠٩﴾

(Kuti akhale) chikumbutso. Ndipo sitidali osalungama (powaononga popanda kuwachenjeza).

وَمَا تَنَزَّلَتْ بِهِ ٱلشَّيَٰطِينُ ﴿٢١٠﴾

Ndipo asatana sadaivumbulutse (iyi Qur’an monga osakhulupirira akunenera monyoza).

وَمَا يَنۢبَغِى لَهُمْ وَمَا يَسْتَطِيعُونَ ﴿٢١١﴾

Ndipo sikoyenera kwa iwo (kuivumbulutsa Qur’an) ndiponso sangathe.

إِنَّهُمْ عَنِ ٱلسَّمْعِ لَمَعْزُولُونَ ﴿٢١٢﴾

Ndithu iwo ngotsekerezedwa kumvetsera (zimene angelo amalankhula kumwamba).

فَلَا تَدْعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَكُونَ مِنَ ٱلْمُعَذَّبِينَ ﴿٢١٣﴾

Choncho usapembedze mulungu wina pamodzi ndi Allah, kuti ungakhale mwa olangidwa.

وَأَنذِرْ عَشِيرَتَكَ ٱلْأَقْرَبِينَ ﴿٢١٤﴾

Ndipo achenjeze abale ako a pafupi.

وَٱخْفِضْ جَنَاحَكَ لِمَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلْمُؤْمِنِينَ ﴿٢١٥﴾

Ndipo fungatira ndi phiko lako amene akutsata mwa okhulupirira. (Ukhale wachifundo kwa iwo).

فَإِنْ عَصَوْكَ فَقُلْ إِنِّى بَرِىٓءٌۭ مِّمَّا تَعْمَلُونَ ﴿٢١٦﴾

Ngati atakunyoza, nena: “Ine ndili kutali ndi zimene mukuchitazo.”

وَتَوَكَّلْ عَلَى ٱلْعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ ﴿٢١٧﴾

Ndipo tsamira kwa (Mbuye wako) Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha.

ٱلَّذِى يَرَىٰكَ حِينَ تَقُومُ ﴿٢١٨﴾

Yemwe akukuona pamene ukuimilira (pamapemphero).

وَتَقَلُّبَكَ فِى ٱلسَّٰجِدِينَ ﴿٢١٩﴾

Ndikutembenukatembenuka kwako (pogwetsa mphumi yako pansi ndi kudzuka ndi kuimilira) pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi (polambira Allah).

إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلْعَلِيمُ ﴿٢٢٠﴾

Ndithu Iye Ngwakumva; Ngodziwa chilichonse.

هَلْ أُنَبِّئُكُمْ عَلَىٰ مَن تَنَزَّلُ ٱلشَّيَٰطِينُ ﴿٢٢١﴾

Kodi ndikuuzeni amene asatana amawatsikira?

تَنَزَّلُ عَلَىٰ كُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٍۢ ﴿٢٢٢﴾

Amamtsikira yense wabodza lamkunkhuniza; wamachimo.

يُلْقُونَ ٱلسَّمْعَ وَأَكْثَرُهُمْ كَٰذِبُونَ ﴿٢٢٣﴾

Amawaponyera (asatana anzawo a mu anthu) zimene azimva. Koma ambiri a iwo ngabodza.

وَٱلشُّعَرَآءُ يَتَّبِعُهُمُ ٱلْغَاوُۥنَ ﴿٢٢٤﴾

Ndipo alakatuli (olakatula zopanda phindu) amatsatidwa ndi (anthu) opotoka.

أَلَمْ تَرَ أَنَّهُمْ فِى كُلِّ وَادٍۢ يَهِيمُونَ ﴿٢٢٥﴾

Kodi suona kuti iwo akungoyumbayumba m’chigwa chilichonse (chamawu)?

وَأَنَّهُمْ يَقُولُونَ مَا لَا يَفْعَلُونَ ﴿٢٢٦﴾

Ndithunso iwo akunena zomwe sachita.

إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَذَكَرُواْ ٱللَّهَ كَثِيرًۭا وَٱنتَصَرُواْ مِنۢ بَعْدِ مَا ظُلِمُواْ ۗ وَسَيَعْلَمُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَىَّ مُنقَلَبٍۢ يَنقَلِبُونَ ﴿٢٢٧﴾

Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, ndikumamtchula Allah mowirikiza, ndikuzipulumutsa okha pambuyo pochitiridwa zoipa. Ndipo posachedwa amene adzichitira okha zoipa adziwa kotembenukira komwe adzatembenukire.